Kusamvera ndi Tsoka
Epic Fantasy

Kusamvera ndi Tsoka

Author

Fr. Kondwani Jabu

Description

Bruno adali galu. Iye adali ndi mbuye wake, wachizungu, Sigerege. Mbuyeyu, ankamukonda kwambiri. Iye ankakhala moyo wofewa. Iye ankagona pakama ndipo adali ndi zofunda. Iye sankagona panja monga momwe agalu ena onse achitira. Iye adali ndi chipinda chake mkati mwa nyumba ya mbuye wake. Koma ufulu wonsewo uli apo, iye ankadandaula kuti adalibe ufulu. Iye ankasirira agalu ena, omwe ankayenda mwachisawawa, komanso ankagona panja ngati adalibe mbuye wawo. Tsiku lina, mbuye wake pomutopera, adamupatsa mwayi wotuluka panja kuti akasangalale , monga momwe agalu ena ankachitira. Atatuluka, Bruno adakumanizana ndi mkango womwe udatsala pang'ono kuuchotsa moyo wake. Zidatengera mbuye wake kuupha ndi mfuti usadamumbwandire.

...

Share this book

Share this book with friends and family