Chibwana Chimalanda
Epic Fantasy

Chibwana Chimalanda

Author

Emmanuel Chiwaya

Description

Chanju adali mwana wa sitandade 8, pasukulu ya Gaga. Iye adali wanzeru zedi, koma wamphulupulu. Koma atalangizidwa, iye adaleka mphulupulu. Atasankhidwa kupita kusekondale, iye adabwereranso ku moyo wake wakale, wamphulupulu. Iye adayamba kuyenda ndi Lumbani, mwana wasukulu yemwe adali wamakhalidwe oipa. Kupyolera n'kuyerekedwa kwawo, awiriwa, adawononga zipangizo zamagetsi a pasukulu yawo, Matowo. Iwo atafunsidwa kuti alipire, Bambo a Lumbani adakwanitsa kulipira, pomwe mayi a Chanju sadakwanitse. Chanju adachotsedwa sukulu, pomwe Lumbani adapitiriza. Patapita zaka zambiri, Chanju, asakudziwa kalikonse, adalembedwa ntchito yaulonda pakampani yomwe bwana wamkulu, adali Lumbani.

...

Share this book

Share this book with friends and family